if you like my content and would like to support me further, please
PayPal
➡️To Donate please use PayPal www.paypal.me/...
Business/Sponsor Inquiries //hanifamw.suggestions@gmail.com
Mu November mchaka cha 2021, pamene mlaliki Shepherd Bushiri pamodzi ndi mkazi wake Mary anathawa belo mdziko la South Africa mkubwera kuno ku Malawi, anthu ambiri anayesa kuti basi watha ndipo sangapangenso chilichonse cholozeka. Hotel yake yotchedwa Sparkling and Spa yomwe ili mu dera wa Rustenburg mdzikolo inayamba kupita pansi popeza malonda sankayenda. Ndalama zomwe amkazipeza kuchoka mu chopereka chaku tchalichi kamba kakuthawaku izi zinayima. Kenako ali ku Malawi analengeza za scholarship yomwe iye akufuna kuthandiza ana osowa fees mma sukulu osiyanasiyana. Apa anthu sanamukhulupilire popeza amkati alibe ndalama ndipo amapanga izi pongofuna kutchuka.
Komatu Bushiri wadabwitsa ndikututumutsa anthu ambiri posachedwapa atalengeza kuti akumanga mzinda m’boma wa Mangochi womwe akuwutcha kuti Goshen City.
Негізгі бет Chifukwa Chenicheni Chomwe Shepherd Bushiri Akumangira Mzinda Wa GOSHEN CITY
Пікірлер: 124