Lyrics:
1. Zosautsa zochuluka okondedwa m'moyowu
Kukumana ndi zipsinjo zosaneneka
Kuyesetsa kupemphera ngati Mlungu saakumva
Zafika povuta moyuwu kuwawa
Kuyang’ana uko wachoka ndizogwetsa mphwayi
Kuganiza zatsogolo mtima umasweka
Nthawi zina ukaona ena zithu zikuwayendera
Zimangopangitsa ‘we kukhumudwa
Chorus
Kaya nyengo ivute iwopse bwanji
Ndi zinthu za kanthawi kanthawi kochepa
Zisakuchotse ‘we pamaso pa Mulengi wako
Khalabe odikira mkhulupire
Akulonjeza kukhala nawe kukusamalira zinthu zikavuta
Ngakhale lonjezano lake lichedwe bwanji
Khalabe odikira mkhulupire
2. Zolilitsa tsiku ndi tsiku kuopsedwa m'moyowu
Kunyozedwa ndiopembedza nao limodzi
Komabe m'nyengo zotere kumbuka liripo bwenzi
Bwenzi lopambana ndiye Yesu
Akhala nawe poyenda akhala nawe pogona
Akhala mawe mtendere ndinso polira
Iye ali ndi chinsisi cha tsogolo la moyo wako
Khalabe odikira mkhulupire
-----------------------------------------------------
The Morning Star, Kawale, Lilongwe
Audio by: Recall, Kuimba Mwamphamvu Studio
Video by: Hope Channel Malawi
-----------------------------------------------------
Share this video:
• Khalabe Odikira - The ...
Subscribe for more videos:
/ @themorningstar-mw
Audio playlist:
• M'bandakucha - The Mor...
-----------------------------------------------------
Connect with us:
Facebook: / themorningstarsingersmw
Instagram: / themorningstar_mw
Whatsapp: whatsapp.com/channel/0029Va5V...
Spotify - spotify.link/EC6GyW0v3xb
E-mail:
themorningstarsingers@gmail.com
Негізгі бет Музыка Khalabe Odikira - The Morning Star (Official Video)
Пікірлер: 109